CRUISE 5 WITH MAI NAYERE JEKETE - 11 APRIL 2021

Sdílet
Vložit
  • čas přidán 13. 04. 2021
  • Mai Nayere Najere ndi mai otchuka kwambiri chifukwa kupatula kukhala mzamba, ndi katswiri othandiza anthu pamavuto awo okhudzana ndi kugonana komanso kubeleka.
    Mai Nayere adayamba ntchito yauzamba mzaka zamma 1980 kutsatila kumwalira kwa mai wao amene amachitanso ntchito yomweyi. Iwo akuti mai awo atamwalira adawaonekela kumaloto komwe adawaululira mankhwala onse.
    Kuyambila pomwepo adayamba kuthandiza amai ndi abambo amene siatha kubeleka, kuthandiza amai kuchila, kuunika mavuto okhudza kubeleka a amai.
    Mai Nayere amakanitsitsa kuti si sing'anga koma dokotala. Akuti iwo saombeza ndipo sapeleka zizimba.
    Pa zina zodabwitsa zomwe maiwa amachita, amatha kuunika mmimba munthu pogwilitsa ntchito galasi ngati logwilitsa ntchito popesa.
    Mai Nayere amapezake ku Lilongwe mmudzi mwa Chipalamnjira, TA Chadza pafupi ndi Nanjiri.
  • Zábava

Komentáře • 94